Pamenepo Mose anatenga mkazi wace ndi ana ace amuna, nawakweza pa buru, nabwerera kumka ku dziko la Aigupto; ndipo Mose anagwira ndodo ya Mulungu m'dzanja lace.