10. Ndipo analumikiza nsaru zisanu yina ndi inzace; nalumikiza nsaru zisanu zina yina ndi inzace.
11. Ndipo anaika magango ansaru yamadzi m'mphepete mwace mwa nsaru imodzi ku mkawo wa cilumikizano; nacita momwemo m'mphepete mwace mwa nsaru ya kuthungo, ya cilumikizano caciwiri.
12. Anaika magango makumi asanu pa nsaru imodzi, naikanso magango makumi asanu m'mphepete mwace mwa nsaru ya cilumikizano cina; magango anakomanizana lina ndi linzace.
13. Ndipo anazipanga zokowera makumi asanu zagolidi, namanga nsaru pamodzi ndi zokowerazo; ndipo kacisi anakhala mmodzi.
14. Ndipo anaomba nsaru zophimba za ubweya wa mbuzi zikhale hema pamwamba pa kacisi; anaomba nsaru zophimba khumi ndi imodzi.
15. Utali wace wa nsaru imodzi ndiwo mikono makumi atatu, ndi kupingasa kwace kwa nsaru imodzi ndiko mikono inai; nsaru khumi ndi imodzi zinafanana muyeso wao.
16. Ndipo anamanga pamodzi nsaru zisanu pa zokha, ndi nsaru zisanu ndi imodzi pa zokha.