1. Ndipo iye ananena ndi Mose, Ukwere kudza kwa Yehova, iwe ndi Aroni, Nadabu ndi Abihu, ndi akuru a Israyeli makumi asanu ndi awiri; ndipo mugwadire pakudza kutali;
2. ndipo Mose yekha ayandikire kwa Yehova; koma asayandikire iwowa; ndi anthunso asakwere naye.
3. Ndipo Mose anadza nafotokozera anthu mau onse a Yehova, ndi masveruzo onse; ndipo anthu onse anabvomera pamodzi, nati, Mau onse walankhula Yehova tidzacita.