Potero imvani, Israyeli, musamalire kuwacita, kuti cikukomereni ndi kuti mucuruke cicurukire, monga Yehova Mulungu wa makolo anu anena ndi inu, m'dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi.