15. Ndi zinthu zoposa za mapiri akale,Ndi zinthu zofunikatu za zitunda zosatha,
16. Ndi zinthu zofunikatu za dziko lapansi, ndi kudzala kwace,Ndi cibvomerezo ca iye anakhala m'citsambayo;Mdalitso ufike pa mutu wa Yosefe,Ndi pakati pa mutu wace wa iye wokhala padera ndi abale ace.
17. Woyamba kubadwa wa ng'ombe yace, ulemerero ndi wace;Nyanga zace ndizo nyanga zanjati;Adzatunga nazo mitundu ya anthu pamodzi, kufikira malekezero a dziko lapansi.Iwo ndiwo zikwi khumi za Efraimu,Iwo ndiwo zikwi za Manase.
18. Ndi za Zebuloni anati,Kondwera, Zebuloni, ndi kuturukakwako;Ndi Isakara, m'mahema mwako.
19. Adzaitana mitundu ya anthu afike kuphiri;Apo adzaphera nsembe za cilungamo;Popeza adzayamwa zocuruka za m'nyanja,Ndi cuma cobisika mumcenga.
20. Ndi za Gadi anati,Wodala iye amene akuza Gadi;Akhala ngati mkango waukazi,Namwetula dzanja, ndi pakati pa mutu pomwe.
21. Ndipo anadzisankhira gawo loyamba,Popeza kumeneko kudasungika gawo la wolamulira;Ndipo anadza ndi mafumu a anthu,Anacita cilungamo ca Yehova,Ndi maweruzo ace ndi Israyeli.
22. Ndi za Dani anati,Dani ndiye mwana wa mkango,Wakutumpha moturuka m'Basana.
23. Za Nafitali anati,Nafitali, wokhuta nazo zomkondweretsa,Wodzala ndi mdalitso wa Yehova;Landira kumadzulo ndi kumwela.
24. Ndi za Aseri anati,Aseri adalitsidwe mwa anawo;Akhale wobvomerezeka mwa abale ace,Abviike phazi lace m'mafuta.
25. Nsapato zako zikhale za citsulo ndi mkuwa;Ndipo monga masiku ako momwemo mphamvu yako.