1. Pamenepo tinabwerera, ndi kuyenda kumka kucipululu, kutsata njira ya Nyanja Yofiira, monga Yehova adanena ndi ine; ndipo tinapaza phiri la Seiri masiku ambiri.
2. Ndipo Yehova ananena ndi ine, ndi kuti,
3. Yakwanira nthawi yakupaza inu phiri ili; tembenukani kumka kumpoto,
4. Ndipo uuze anthu, ndi kuti, Mukapite kubzyola malire a abale anu, ana a Bsau okhala m'Seiri; ndipo adzakuopani; mucenjere ndithu;
5. musalimbana nao; popeza sindikupatsakoni dziko lao, pangakhale popondapo phazi lanu ai pakuti ndapatsa Bsau phiri la Seiri likhale lace lace.
6. Mugulane nao cakudya ndi ndarama, kuti mudye; mugulane naonso madzi kuti mumwe.
7. Pakuti Yehova Mulungu wanu anakudalitsani mu nchito zonse za manja anu; anadziwa kuyenda kwanu m'cipululu ici cacikuru; zaka izi makumi anai Yehova Mulungu wanu anakhala ndi inu; simunasowa kanthu.