1. Tsoka osalabadirawo m'Ziyoni, ndi iwo okhazikika m'phiri la Samariya, ndiwo anthu omveka amtundu woposa wa anthu, amene nyumba ya Israyeli iwafikira!
2. Pitani ku Kaline, nimuone; kucokera komweko mupite ku Hamati wamkulu mutsikire ku Gati wa Afilisti; kodi awo ndi okoma koposa maufumu ano? kapena malire ao aposa malire anu?
3. Inu akutalikitsa tsiku loipa, ndi kusendeza pafupi mpando waciwawa;
4. ogona pa makama aminyanga, nadzithinula pa maguwa ao ogonapo, nadya ana a nkhosa a ku zoweta, ndi ana a ng'ombe ocoka pakati pa khola;
5. akungoyimba kutsata maliridwe a zeze, nadzilingiririra zoyimbira nazo Ingati Davide;
6. akumwera vinyo m'zipanda, nadzidzoza ndi mafuta abwino oposa, osagwidwa cisoni ndi kutyoka kwa Yosefe.
7. Cifukwa cace tsono, adzatengedwa ndende ndi oyamba kutengedwa ndende; ndi phokoso la iwo odzithinula lidzapita.
8. Ambuye Yehova walumbira pali Iye mwini, ati Yehova Mulungu wa makamu, Ndinyansidwa nako kudzikuza kwa Yakobo, ndidana nazo nyumba zace zacifumu; m'mwemo ndidzapereka mudzi, ndi zonse ziri m'menemo.
9. Ndipo kudzacitika, mukatsala amuna khumi m'nyumba imodzi, adzafa.