Comweco Yehova anatumiza mliri pa Israyeli kuyambira m'mawa kufikira nthawi yoikika; ndipo anafapo anthu zikwi makumi asanu ndi awiri kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba.