6. Koma oipa onse adzakhala ngati minga yoyenera kuitaya,Pakuti siigwiridwa ndi dzanja;
7. Koma wakukhudza iyo adzikonzeratu citsulo ndi luti la mkondo;Ndipo idzatenthedwa konse ndi mota m'malo mwao.
8. Maina a ngwazi Davide anali nazo ndiwo: Josebu-basebete Mtakemoni, mkuru wa akazembe; ameneyu ndiye Adino M-ezni wolimbana ndi mazana atatu ophedwa nthawi imodzi.
9. Ndipo wotsatana naye Eleazeri mwana wa Dodai mwana wa M-akohi, mmodzi wa ngwazi zitatu zokhala ndi Davide pamene iwo anatonza Afilisti osonkhanidwa kunkhondo kumeneko, atacoka Aisrayeli;