Ndipo anyamata a Abisalomu anafika kunyumba kwa mkaziyo; nati, Ali kuti Ahimaazi ndi Jonatani? Ndipo mkaziyo ananena nao, Anaoloka kamtsinje kamadzi. Ndipo atawafunafuna, osawapeza, anabwerera kumka ku Yerusalemu.