Cifukwa cace tsono cakuti ndadzanena mau awa ndi mbuye wanga mfumu, ndico kuti anthu anandiopsa ine; ndipo mdzakazi wanu ndinati, Ndilankhuletu ndi mfumu; kapena mfumu idzacita copempha mdzakazi wace.