Ndipo pakuturuka malirowo, Davide anatumiza munthu namtenga afike kwao ku nyumba yace; ndipo iyeyo anakhala mkazi wace nambalira mwana wamwamuna. Koma Yehova anaipidwa ndi cinthu cimene Davide adacita.