Ndipo Kore mwana wa Imna Mlevi, wa ku cipata ca kum'mawa, anayang'anira zopereka zaufulu za Mulungu, kugawira nsembe zokweza za Yehova, ndi zopatulikitsa.