Ndipo mfumu ndi Yehoyada anazipereka kwa iwo akugwira nchito ya utumiki ya nyumba ya Yehova, nalembera amisiri omanga ndi miyala, ndi osema mitengo, akonzenso nyumba ya Yehova; ndiponso akucita ndi citsulo ndi mkuwa alimbitse nyumba ya Yehova.