Ndipo pofunsa mfumu, mkaziyo anaisimbira. Pamenepo mfumu anamuikira mdindo, ndi kuti, Bwezetsa zace zonse ndi zipatso zonse za m'munda, cicokere iye m'dziko mpaka lero lino.