Naturutsa kucotsa komweko cuma conse ca nyumba ya Yehova, ndi cuma ca nyumba ya mfumu, naduladula zipangizo zonse zagolidi adazipanga Solomo mfumu ya Israyeli m'Kacisi wa Yehova, monga Yehova adanena.