Pakufika iye, onani, Eli analikukhala pampando m'mbali mwa njira, alikuyang'anira, popeza mtima wace unanthunthumira cifukwa ca likasa la Mulungu, Pamene munthu uja anafika m'mudzimo, nanena izi, a m'mudzi monse analira.