9. Comweco Davide anamuka, iye ndi anthu mazana asanu ndi limodzi anali naye, nafika kukamtsinje Besori, pamenepo anatsala ena.
10. Ndipo Davide anawalondola, iye ndi anthu mazana anai; koma anthu mazana awiri anatsala m'mbuyo, cifukwa analema, osakhoza kuoloka kamtsinje Besori.
11. Ndipo ena anapeza M-aigupto kuthengo, nabwera naye kwa Davide, nampatsa cakudya, nadya iye; nampatsanso madzi kumwa;
12. nampatsanso cigamphu ca ncinci ya nkhuyu ndi ncinci ziwiri za mphesa; ndipo atadya, moyo wace unabweranso mwa iye; pakuti adagona masiku atatu ndi usiku wao, osadya cakudya, osamwa madzi.
13. Pamenepo Davide ananena naye, Ndiwe wa yani? ufumira kuti? Nati iye, Ndiri mnyamata wa ku Aigupto, kapolo wa M-amaleki; mbuye wanga anandisiya, cifukwa ndinayambodwala apita masiku atatu.
14. Tinathira nkhondo kumwera kwa Akereti ndi ku dziko lija la Ayuda, ndi kumwera kwa Kalebi; ndipo tinatentha mudzi wa Zikilaga ndi moto.