Cifukwa cace Eli anati kwa Samueli, Pita, ukagone; ndipo akakuitananso, ukabvomere, kuti, Nenani, Yehova, popeza mnyamata wanu akumva. Comweco Samueli anakagona m'malo mwace.