Tsono iwo awiri anagawana dziko kukaliyendera; Ahabu anadzera njira yace yekha, ndi Obadiya njira yina yekha.