Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yuda 1:14-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo kwa iwo, Henoke, wacisanu ndi ciwiri kuyambira kwa Adamu, ananenera kuti, Taona, wadza Ambuye ndi oyera ace zikwi makumi,

15. kudzacitira onse ciweruziro, ndi kutsutsa osapembedza onse, pa nchito zao zonse zosapembedza, zimene anazicita kosapembedza, ndi pa zolimba zimene ocimwa osapembedza adalankhula pa iye.

16. Amenewo ndiwo odandaula, oderera, akuyenda monga mwa zilakolako zao (ndipo pakamwa pao alankhula zazikuruzikuru), akutama anthu cifukwa ca kupindula nako.

17. Koma inu, abale, mukumbukile mau onenedwa kale ndi atumwi a Ambuye wathu Yesu Kristu;

18. kuti ananena nanu, 1 Pa nthawi yotsiriza padzakhala otonza, akuyenda monga mwa zilakolako zosapembedza za iwo okha.

19. Iwo ndiwo opatukitsa, anthu a makhalidwe acibadwidwe, osakhala naye Mzimu.

20. Koma inu, okondedwa, 3 podzimangirira nokha pa cikhulupiriro canu coyeretsetsa, ndi 4 kupemphera mu Mzimu Woyera,

21. mudzisunge nokha m'cikondi ca Mulungu, ndi 5 kulindira cifundo ca Ambuye wathu Yesu Kristu, kufikira moyo wosatha.

22. Ndipo ena osinkhasinkha muwacitire cifundo,

23. koma ena 6 muwapulumutse ndi kuwakwatula kumoto; koma ena muwacitire cifundo ndi mantha, 7 nimudane naonso maraya ocitidwa mawanga ndi thupi

24. Ndipo 8 kwa iye amene akhoza kukudikirani mungakhumudwe, ndi 9 kukuimikani pamaso pa ulemerero wace opanda cirema m'kukondwera,

25. 10 kwa Mulungu wayekha, Mpulumutsi wathu, mwa Yesu Kristu Ambuye wathu, zikhale ulemerero, ukulu, mphamvu, ndi ulamuliro zisanayambe nthawi, ndi tsopano, ndi kufikira nthawi zonse. Amen.

Werengani mutu wathunthu Yuda 1