Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 9:4-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Tiyenera kugwira nchito za iye wondituma Ine, pokhala pali msana; ukudza usiku pamene palibe munthu angakhoze kugwira nchito,

5. Pakukhala Ine m'dziko lapansi, ndiri kuunika kwa dziko lapansi.

6. Pamene ananena izi, analabvula pansi, nakanda thope ndi malobvuwo, napaka thopelo m'maso,

7. nati kwa iye, Muka, kasambe m'thamanda la Siloamu (ndilolosandulika, Wotumidwa). Pamenepo anacoka, nasamba, nabwera alikuona.

8. Cifukwa cace anzace ndi iwo adamuona kale, kuti anali wopemphapempha, ananena, Kodi si uyu uja wokhala ndi kupemphapempha?

9. Ena ananena, kuti, Ndiyeyu; ena ananena, lai, koma afanana naye. Iyeyu anati, Ndine amene.

10. Pamenepo ananena ndi iye, Nanga maso ako anatseguka bwanji?

11. Iyeyu anayankha, Munthuyo wochedwa Yesu anakanda thope, napaka m'maso mwanga, nati kwa ine, Muka ku Siloamu kasambe; cifukwa cace ndinacoka, ndipo m'mene ndinasamba ndinapenya,

12. Ndipo anati kwa iye, Ali kuti Iyeyo? Anena, Sindidziwa ine.

13. Anapita naye amene anali wosaona kale kwa Afarisi.

14. Koma tsikulo ndi la Sabata limene Yesu anakanda thope, namtsegulira iye maso ace.

15. Pamenepo ndipo Afarisi anamfunsanso, umo anapenyera, Ndipo anati kwa iwo, Anapaka thope m'maso mwanga, ndinasamba, ndipo ndipenya.

16. Ena pamenepo mwa Afarisi ananena, Munthu uyu sacokera kwa Mulungu, cifukwa sasunga Sabata. Koma ena ananena, Munthu ali wocimwa, akhoza bwanji kucita zizindikilo zotere? Ndipo panali kutsutsana mwa iwo.

Werengani mutu wathunthu Yohane 9