Ena pamenepo mwa Afarisi ananena, Munthu uyu sacokera kwa Mulungu, cifukwa sasunga Sabata. Koma ena ananena, Munthu ali wocimwa, akhoza bwanji kucita zizindikilo zotere? Ndipo panali kutsutsana mwa iwo.