Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 9:14-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Koma tsikulo ndi la Sabata limene Yesu anakanda thope, namtsegulira iye maso ace.

15. Pamenepo ndipo Afarisi anamfunsanso, umo anapenyera, Ndipo anati kwa iwo, Anapaka thope m'maso mwanga, ndinasamba, ndipo ndipenya.

16. Ena pamenepo mwa Afarisi ananena, Munthu uyu sacokera kwa Mulungu, cifukwa sasunga Sabata. Koma ena ananena, Munthu ali wocimwa, akhoza bwanji kucita zizindikilo zotere? Ndipo panali kutsutsana mwa iwo.

17. Pamenepo ananenanso kwa wosaonayo, Iwe unenanji za iye, popeza anakutsegulira maso ako? Koma iye anati, Ali Mneneri.

18. Cifukwa cace Ayuda sanakhulupirira za iye, kuti anali wosaona, napenya, kufikira kumene adaitana atate wace ndi amace a iye wopenya;

19. nawafunsa iwo, nanena, Kodi uyu ndi mwana wanu, amene inu munena kuti anabadwa wosaona?

20. Ndipo apenya bwanji tsopano? Atate wace ndi amace anayankha nati, Tidziwa kuti uyu ndi mwana wathu, ndi kuti anabadwa wosaona;

21. koma sitidziwa umo apenyera tsopano; kapena sitimdziwa amene anamtsegulira pamaso pace; mumfunse iye; ali wamsinkhu; adzalankhula mwini za iye yekha.

22. Izi ananena atate wace ndi amace, cifukwa anaopa Ayuda; pakuti Ayuda adapangana kale, kuti ngati munthu ali yense adzambvomereza iye kuti ndiye Kristu, akhale woletsedwa m'sunagoge,

23. Cifukwa ca ici atate wace ndi amace anati, Ali wamsinkhu; mumfunse iye.

24. Pamenepo anamuitana kaciwiri munthuyo amene anali wosaona, nati kwa iye, Lemekeza Mulungu; tidziwa kuti munthuyo ali wocimwa.

25. Pamenepo iyeyu anayankha, Ngati ali wocimwa, sindidziwa; cinthu cimodzi ndicidziwa, pokhala ndinali wosaona, tsopano ndipenya.

26. Cifukwa cace anati kwa iye, Anakucitira iweciani? anakutsegulira iwe maso bwanji?

27. Iye anayankha iwo, Ndinakuuzani kale, ndipo simunamva; mufuna kumvanso bwanji? kodi inunso mufuna kukhala: akuphunzira ace?

Werengani mutu wathunthu Yohane 9