Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 9:11-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Iyeyu anayankha, Munthuyo wochedwa Yesu anakanda thope, napaka m'maso mwanga, nati kwa ine, Muka ku Siloamu kasambe; cifukwa cace ndinacoka, ndipo m'mene ndinasamba ndinapenya,

12. Ndipo anati kwa iye, Ali kuti Iyeyo? Anena, Sindidziwa ine.

13. Anapita naye amene anali wosaona kale kwa Afarisi.

14. Koma tsikulo ndi la Sabata limene Yesu anakanda thope, namtsegulira iye maso ace.

15. Pamenepo ndipo Afarisi anamfunsanso, umo anapenyera, Ndipo anati kwa iwo, Anapaka thope m'maso mwanga, ndinasamba, ndipo ndipenya.

16. Ena pamenepo mwa Afarisi ananena, Munthu uyu sacokera kwa Mulungu, cifukwa sasunga Sabata. Koma ena ananena, Munthu ali wocimwa, akhoza bwanji kucita zizindikilo zotere? Ndipo panali kutsutsana mwa iwo.

17. Pamenepo ananenanso kwa wosaonayo, Iwe unenanji za iye, popeza anakutsegulira maso ako? Koma iye anati, Ali Mneneri.

18. Cifukwa cace Ayuda sanakhulupirira za iye, kuti anali wosaona, napenya, kufikira kumene adaitana atate wace ndi amace a iye wopenya;

19. nawafunsa iwo, nanena, Kodi uyu ndi mwana wanu, amene inu munena kuti anabadwa wosaona?

20. Ndipo apenya bwanji tsopano? Atate wace ndi amace anayankha nati, Tidziwa kuti uyu ndi mwana wathu, ndi kuti anabadwa wosaona;

Werengani mutu wathunthu Yohane 9