Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 8:9-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Koma iwo, m'mene adamva, anaturukamo amodzi amodzi, kuyambira akulu, kufikira otsiriza; ndipo Yesu anatsala yekha, ndi mkazi, alikuima pakati.

10. Koma Yesu pamene adaweramuka, anati kwa iye, Mkazi iwe, ali kuti ajawa? Palibe munthu anakutsutsa kodi?

11. Koma iye anati, Palibe, Ambuye. Ndipo Yesu anati, Inenso sindikutsutsa iwe; pita; kuyambira tsopano usacimwenso.

12. Pamenepo Yesu analankhulanso nao, nanena, Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.

13. Cifukwa cace Afarisi anati kwa iye, Mucita umboni wa Inu nokha; umboni wanu suli woona.

14. Anayankha Yesu nati kwa iwo, Ndingakhale ndicita umboni wa Ine ndekha umboni wanga uli woona; cifukwa ndidziwa kumene ndinacokera ndi kumene ndimukako; koma e inu, simudziwa kumene ndicokera, ndi kumene ndimukako.

15. Inu muweruza monga mwa thupi; Ine sindiweruza munthu.

16. Ndipo ngati ndiweruza Ine, ciweruziro canga ciri coona; pakuti sindiri pa ndekha, koma ine ndi Atate amene anandituma Ine.

17. Inde kudalembedwa m'cilamulo canu kuti umboni wa anthu awiri uli woona.

18. Ine ndine wakucita umboni wa Ine ndekha, ndipo Atate amene anandituma Ine, acita umboni wa Ine.

19. Cifukwa cace ananena ndi iye, Ali kuti Atate, wanu? Yesu anayankha, Simudziwa kapena Ine, kapena Atate wanga; mukadadziwa Ine, mukada-dziwanso Atate wanga.

20. Mau awa analankhula m'nyumba ya cuma ca Mulungu pophunzitsa m'Kacisi; ndipo palibe munthu anamgwira iye, pakuti nthawi yace siinafike.

21. Pamenepo anatinso kwa iwo; Ndimuka Ine, ndipo mudzandifuna, ndipo m'cimo lanu mudzafa: kumene ndimukako Ine, simudziwa kudza inu.

22. Cifukwa cace Ayuda ananena, Kodi adzadzipha yekha, pakuti ananena, Kumene ndimukako Ine, simudziwa inu kudza?

23. Ndipo ananena nao, Inu ndinu ocokera pansi; Ine ndine wocokera Kumwamba; inu ndinu a dziko lino lapansi; sindiri Ine wa dziko lino lapansi.

24. Cifukwa cace ndinati kwa inu, kuti mudzafam'macimo anu, pakuti ngati simukhulupirira kuti Ine ndine, mudzafa m'macimo anu.

25. Pamenepo ananena kwa iye, Ndinu yani? Yesu anati kwa iwo, Cimene comwe ndidalankhulanso ndi inu kuyambira paciyambi.

Werengani mutu wathunthu Yohane 8