Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 7:8-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. K werani inu kunka kuphwando; sindikwera Ineku phwando ili tsopano apa; pakuti nthawi yanga siinakwanire.

9. Ndipo m'mene adanena nao zimenezi anakhalabe m'Galileya,

10. Koma pamene abale ace adakwera kunka kuphwando, pomwepo Iyenso anakwera, si poonekera, koma monga mobisalika.

11. Pomwepo Ayuda analikumfuna iye paphwando, nanena, Ali kuti uja?

12. Ndipo kunali kung'ung'udza kwambiri za iye m'makamu a anthu; ena ananena, kuti, Ali wabwino; koma ena ananena, lai, koma asoceretsa khamu la anthuwo.

13. Cinkana anatero panalibe munthu analankhula za iye poyera, cifukwa ca kuopa Ayuda.

14. Koma pamene padafika pakati pa phwando, Yesu anakwera nalowa m'Kacisi, naphunzitsa,

15. Cifukwa cace Ayuda anazizwa, nanena, Ameneyu adziwa bwanji zolemba, wosaphunzira?

16. Pamenepo Yesu anayankha iwo, nati, Ciphunzitso canga siciri canga, koma ca iye amene anandituma Ine.

17. Ngati munthu ali yense afuna kucita cifuniro cace, adzazindikira za ciphunzitsoco, ngati cicokera kwa Mulungu, kapena ndilankhula zocokera kwa Ine ndekha.

18. Iye wolankhula zocokera kwa iye yekha afuna ulemu wa mwini yekha, iye wakufuna ulemu wa iye amene anamtuma, yemweyu ali woona, ndipo mwa iye mulibecosalungama.

19. Si Mose kodi anakupatsani inu cilamulo, ndipo kulibe mmodzi mwa inu acita cilamulo? Mufuna kundipha cifukwa ninji?

20. Khamu la anthu linayankha, Muli ndi ciwanda: afuna ndani kukuphani lou?

21. Yesu anayankha nati kwa iwo, Ndinacita nchito imodzi, ndipo muzizwa monse,

Werengani mutu wathunthu Yohane 7