Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 7:20-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Khamu la anthu linayankha, Muli ndi ciwanda: afuna ndani kukuphani lou?

21. Yesu anayankha nati kwa iwo, Ndinacita nchito imodzi, ndipo muzizwa monse,

22. Cifukwa ca ici Mose, anakupatsani inu mdulidwe (si kuti ucokera kwa Mose, koma kwa, makolo); ndipo mudula munthu tsiku la Sabata.

23. Ngati munthu alandira mdulidwe tsiku la Sabata, kuti cilamulo ca Mose cingapasulidwe; kodi mundikwiyira Ine, cifukwa ndamciritsadi munthu tsiku la Sabata?

24. Musaweruze monga maonekedwe, koma weruzani ciweruziro colungama.

25. Pamenepo ena a iwo a ku Yerusalemu ananena, Kodi suyu amene afuna kumupha r

26. ndipo taona amalankhula poyera, ndipo sanena kanthu kwa iye. Kapena kodi akuru adziwa ndithu kuti ndiye Kristu ameneyo?

27. Koma ameneyo tidziwa uko acokera: koma Kristu pamene akadzadza, palibe mmodzi adzadziwa uko acokera.

28. Pamenepo Yesu anapfuula m'Kacisi, alikuphunzitsa ndi kunena, Mundidziwa Ine, ndiponso mudziwa uko ndicokera; ndipo sindinadza Ine ndekha, koma iye wondituma Ine amene inu simumdziwa, ali woona.

29. Ine ndimdziwa iye; cifukwa ndiri wocokera kwa iye, nandituma Ine Iyeyu.

30. Pamenepo anafuna kumgwira iye; koma palibe wina anamgwira kumanja, cifukwa nthawi yace siinafike.

31. Koma ambiri a m'khamu la anthu anakhulupirira iye; ndipo ananena, Pamene Kristu akadza kodi adzacita zizindikilo zambiri zoposa zimene adazicita ameneyo?

32. Afarisi anamva khamu la anthu ling'ung'udza zimenezi za iye; ndipo ansembe akulu ndi Afarisi anatuma anyamata kuti akamgwire iye.

Werengani mutu wathunthu Yohane 7