Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 7:2-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Koma phwando la Ayuda, phwando la misasa, linayandikira.

3. Cifukwa cace abale ace anati kwa iye, Cokani pano, mumuke ku Yudeya, kuti akuphunzita anunso akapenye nchito zanu zimenemucita.

4. Pakuti palibe munthu acita kanthu mobisika, nafuna yekha kukhala poyera, Ngati mucita izi, dzionetsereni eni nokha kwa dziko lapansi,

5. Pakuti angakhale abale ace sanakhulupirira iye.

6. Cifukwa cace Yesu ananena nao, Nthawi yanga siinafike; koma nthawi yanu yakonzeka masiku onse.

7. Dziko lapansi silingathe kudana ndi inu; koma Ine lindida popeza Ine ndilicitira umboni, kuti nchito zace ziri zoipa,

8. K werani inu kunka kuphwando; sindikwera Ineku phwando ili tsopano apa; pakuti nthawi yanga siinakwanire.

9. Ndipo m'mene adanena nao zimenezi anakhalabe m'Galileya,

10. Koma pamene abale ace adakwera kunka kuphwando, pomwepo Iyenso anakwera, si poonekera, koma monga mobisalika.

11. Pomwepo Ayuda analikumfuna iye paphwando, nanena, Ali kuti uja?

12. Ndipo kunali kung'ung'udza kwambiri za iye m'makamu a anthu; ena ananena, kuti, Ali wabwino; koma ena ananena, lai, koma asoceretsa khamu la anthuwo.

13. Cinkana anatero panalibe munthu analankhula za iye poyera, cifukwa ca kuopa Ayuda.

14. Koma pamene padafika pakati pa phwando, Yesu anakwera nalowa m'Kacisi, naphunzitsa,

15. Cifukwa cace Ayuda anazizwa, nanena, Ameneyu adziwa bwanji zolemba, wosaphunzira?

16. Pamenepo Yesu anayankha iwo, nati, Ciphunzitso canga siciri canga, koma ca iye amene anandituma Ine.

17. Ngati munthu ali yense afuna kucita cifuniro cace, adzazindikira za ciphunzitsoco, ngati cicokera kwa Mulungu, kapena ndilankhula zocokera kwa Ine ndekha.

18. Iye wolankhula zocokera kwa iye yekha afuna ulemu wa mwini yekha, iye wakufuna ulemu wa iye amene anamtuma, yemweyu ali woona, ndipo mwa iye mulibecosalungama.

Werengani mutu wathunthu Yohane 7