Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 7:11-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Pomwepo Ayuda analikumfuna iye paphwando, nanena, Ali kuti uja?

12. Ndipo kunali kung'ung'udza kwambiri za iye m'makamu a anthu; ena ananena, kuti, Ali wabwino; koma ena ananena, lai, koma asoceretsa khamu la anthuwo.

13. Cinkana anatero panalibe munthu analankhula za iye poyera, cifukwa ca kuopa Ayuda.

14. Koma pamene padafika pakati pa phwando, Yesu anakwera nalowa m'Kacisi, naphunzitsa,

15. Cifukwa cace Ayuda anazizwa, nanena, Ameneyu adziwa bwanji zolemba, wosaphunzira?

16. Pamenepo Yesu anayankha iwo, nati, Ciphunzitso canga siciri canga, koma ca iye amene anandituma Ine.

Werengani mutu wathunthu Yohane 7