Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 6:43-55 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

43. Yesu anayankha nati kwa iwo, Musang'ung'udze winandi mnzace.

44. Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine amkoka iye; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomariza.

45. Calembedwa mwa aneneri, Ndipo adzakhala onse ophunzitsidwa ndi Mulungu. 1 Yense amene adamva kwa Atate, naphunzira, adza kwa Ine.

46. 2 Sikuti munthu wina waona Atate, koma 3 iye amene ali wocokera kwa Mulungu, ameneyo waona Atate.

47. Indetu, indetu, ndinena ndi inu, 4 iye wokhuluplra ali nao moyo wosatha.

48. 5 Ine ndine mkate wamoyo,

49. 6 Makolo anu adadya m'cipululu, ndipo adamwalira.

50. 7 Mkate wotsika Kumwamba ndi uwu, kuti munthu akadyeko ndi kusamwalira.

51. 8 Mkate wamoyo wotsika Kumwamba Ndine amene. Ngati munthu wina akadyako mkate umene, adzakhala ndi moyo kosatha. Inde, ndipo 9 mkate umene ndidzapatsa Ine, ndiwo thupi langa, ukhale moyo wa dziko lapansi.

52. Pamenepo Ayuda anatetana wina ndi mnzace ndi kunena, Akhoza bwanji ameneyu kutipatsa ife kudya thupi lace?

53. Cifukwa cace Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinenandi inu, 10 Ngati simukudya thupi la Mwana wa munthu ndi kumwa mwazi wace, mulibe moyo mwa inu nokha.

54. 11 Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga ali nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomariza.

55. Pakuti thupi langa ndi cakudya ndithu, ndi mwazi wanga ndi caku mwa ndithu.

Werengani mutu wathunthu Yohane 6