Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 6:33-44 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. Pakuti mkate wa Mulungu ndiye wakutsika kucokera Kumwamba ndi kupatsa moyo kwa dziko lapansi.

34. Pamenepo anati kwa iye, Ambuye, tipatseni ife mkate umene nthawi zonse.

35. Yesu anati kwa iwo, Ine ndine mkate wamoyo; iye amene adza kwa Ine sadzamva njala, ndi iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu nthawi zonse.

36. Koma ndinati kwa inu, kuti mungakhale mwandiona, simukhulupirira.

37. Cinthu conse cimene anandipatsa Ine Atate cidzadza kwa Ine; ndipo wakudza kwa Ine sindidzamtaya iye kunja.

38. Pakuti ndinatsika Kumwamba, si kuti ndicite cifuniro canga, koma cifuniro ca iye amene anandituma Ine.

39. Koma cifuniro ca Iye amene anandituma Ine ndi ici, kuti za ici conse Iye anandipatsa Ine ndisatayeko kanthu, koma ndiciukitse tsiku lomariza.

40. Pakuti cifuniro ca Atate wanga ndi ici, kuti yense wakuyang'ana Mwana, ndi kukhulupirira iye, akhale nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomariza.

41. Cifukwa cace Ayuda anang'ung'udza za iye, cifukwa anati, Ine ndine mkate wotsika Kumwamba.

42. Ndipo iwo ananena, Si Yesu uyu, mwana wa Yosefe, atate wace ndi amai wace tiwadziwa? Anena bwanji tsopano, kuti, Ndinatsika Kumwamba?

43. Yesu anayankha nati kwa iwo, Musang'ung'udze winandi mnzace.

44. Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine amkoka iye; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomariza.

Werengani mutu wathunthu Yohane 6