32. Wocita umboni wa Ine ndi wina; ndipo ndidziwa kuti umboni umene iye andicitira Ine uli woona.
33. Inu munatuma kwa Yohane, ndipo iye anacitira umboni coonadi.
34. Ndipo Ine sindilandira umboni kwa munthu: koma ndinena izi, kuti inu mukapulumutsidwe.
35. Iyeyo anali nyali yoyaka ndi yowala; ndipo inu munafuna kukondwera m'kuunika kwace kanthawi.
36. Koma Ine ndiri nao umboni woposa wa Yohane; pakuti nchito zimene Atateanandipatsa ndizitsirize, nchito zomwezo ndizicita zindicitira umboni, kuti Atate anandituma Ine.
37. Ndipo Atate wonditumayo, 1 Iyeyu wandicitira Ine umboni. Simunamva mau ace konse, kapena maonekedwe ace simunaona.
38. Ndipo mulibe mau ace okhala mwa inu; cifukwa kuti amene Iyeyu anatuma, inu simumkhulupirira ameneyo.
39. 2 Musanthula m'malembo, popeza muyesa kuti momwemo muli nao moyo wosatha; ndipo akundicitira Ine umboni ndi iwo omwewo;
40. ndipo 3 simufuna kudza kwa Ine, kuti mukhale nao moyo.
41. 4 Ulemu sindiulandira kwa anthu.
42. Koma ndikudziwani inu, kuti mulibe cikondiea Mulungu mwa inu nokha.
43. Ndadza Ine m'dzina la Atate wanga, ndipo simundilandira Ine; akadza wina m'dzina lace la iye mwini, iyeyu mudzamlandira.
44. Mungathe inu bwanji kukhulupira, 5 popeza mulandira ulemu wina kwa mnzace ndipo ulemu wakucokera kwa Mulungu yekha simuufuna?
45. Musayesa kuti Ine ndidzakunenezani inu kwa Atate; 6 pali wakukunenezani, ndiye Mose, amene inu mumtama.