Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 5:15-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Munthuyo anacoka, nauza Ayuda, kuti ndiye Yesu amene adameiritsa.

16. Ndipo cifukwa ca ici Ayuda analondalonda Yesu, popeza anacita izo dzuwa la Sabata.

17. Koma Yesu anayankha iwo, Atate wanga amagwira nchito kufikira tsopano, lnenso ndigwira nchito.

18. Cifukwa ca ici Ayuda anaonjeza kufuna kumupha, si cifukwa ca kuswa dzuwa la Sabata kokha, komatu amaehanso Mulungu Atate wace wa iye yekha; nadziyesera wolingana ndi Mulungu.

19. Pamenepo Yesu anayankha nati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, sakhoza Mwana kucita kanthu pa yekha, koma cimene aona Atate acicita, ndico. Pakuti zimene iye azicita, zomwezo Mwananso azicita momwemo.

20. Pakuti Atate akonda Mwana, namuonetsa zonse azicita yekha: ndipo adzamuonetsa nchito zoposa izi, kuti mukazizwe,

21. Pakuti monga Atate aukitsa akufa, nawapatsa moyo, momwemonso Mwanaapatsa moyo iwo amene iye afuna.

Werengani mutu wathunthu Yohane 5