Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 5:13-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Koma wociritsidwayo sanadziwa ngati ndani; pakuti Yesu anacoka kacetecete, popeza panali anthu aunyinji m'malo muja.

14. Zitapita izi Yesu anampeza m'Kacisi, nati kwa iye, Taona, waeiritsidwa; usacimwenso, kuti cingakugwere ecipa coposa.

15. Munthuyo anacoka, nauza Ayuda, kuti ndiye Yesu amene adameiritsa.

16. Ndipo cifukwa ca ici Ayuda analondalonda Yesu, popeza anacita izo dzuwa la Sabata.

17. Koma Yesu anayankha iwo, Atate wanga amagwira nchito kufikira tsopano, lnenso ndigwira nchito.

18. Cifukwa ca ici Ayuda anaonjeza kufuna kumupha, si cifukwa ca kuswa dzuwa la Sabata kokha, komatu amaehanso Mulungu Atate wace wa iye yekha; nadziyesera wolingana ndi Mulungu.

19. Pamenepo Yesu anayankha nati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, sakhoza Mwana kucita kanthu pa yekha, koma cimene aona Atate acicita, ndico. Pakuti zimene iye azicita, zomwezo Mwananso azicita momwemo.

Werengani mutu wathunthu Yohane 5