Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 3:5-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu.

6. Cobadwa m'thupi cikhala thupi, ndipo cobadwa mwa Mzimu, cikhala mzimu.

7. Usadabwe cifukwa ndinati kwa iwe, Uyenera kubadwa mwatsopano.

8. Mphepo iomba pomwe ifuna, ndipo ukumva mau ace, komavsudziwa, kumene icokera, ndi kumene imuka; cotero ali yense wobadwa mwa Mzimu.

9. Nikodemo anayankha nati kwa iye, Izi zingatheke bwanji?

10. Yesu anayankha nati kwa iye, Kodi uli mphunzitsi wa Israyeli, ndipo sudziwa izi?

11. Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Tilankhula cimene ticidziwa, ndipo ticita umboni za cimene taeiona; ndipo umboni wathu simuulandira.

12. Ngati ndakuuzani za pansi pano, ndipo simukhulupira, mudzakhulupira bwanji, ngati ndikuuzani za Kumwamba?

13. Ndipo kulibe munthu anakwera Kumwamba, koma iye wotsikayo kucokera Kumwamba, ndiye Mwana wa munthu, wokhala m'Mwambayo.

14. Ndipo monga Mose anakweza njoka m'cipululu, cotero Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa;

15. kuti yense wakukhulupira akhale nao moyo wosatha mwa iye.

16. Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wace wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.

17. Pakuti Mulungu sanatuma Mwana wace ku dziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi iye.

18. Wokhulupirira Iye saweruzidwa; wosakhulupira waweruzidwa ngakhale tsopano, cifukwa sanakhulupirira dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.

19. Koma ciweruziro ndi ici, kuti kuunika kunadza ku dziko lapansi, ndipo anthu anakonda mdima koposa kuunika; pakuti nchito zao zinali zoipa.

Werengani mutu wathunthu Yohane 3