Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 3:15-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. kuti yense wakukhulupira akhale nao moyo wosatha mwa iye.

16. Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wace wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.

17. Pakuti Mulungu sanatuma Mwana wace ku dziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi iye.

18. Wokhulupirira Iye saweruzidwa; wosakhulupira waweruzidwa ngakhale tsopano, cifukwa sanakhulupirira dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.

19. Koma ciweruziro ndi ici, kuti kuunika kunadza ku dziko lapansi, ndipo anthu anakonda mdima koposa kuunika; pakuti nchito zao zinali zoipa.

20. Pakuti yense wakucita zoipa adana nako kuunika, ndipo sakudza kwa kuunika, kuti zingatsutsidwe nchito zace.

21. Koma wocita coonadi adza kukuunika, kuti nchito zace zionekere kuti zinacitidwa mwa Mulungu.

22. Zitapita in anadza Yesu ndi akuphunzira ace ku dziko la Yudeya; ndipo pamenepo anatsotsa nao pamodzi, nabatiza.

23. Ndipo Yohane analinkubatiza m'Ainoni pafupi pa Salemu, cifukwa panali madzi ambiri pamenepo; ndipo analinkufikako anthu, nalinkubatizidwa.

24. Pakuti Yohane sanaikidwe m'ndende.

25. Pamenepo padauka kufunsana mwa ophunzira ace a Yohane ndi Myuda za mayeretsedwe.

26. Ndipo anadza kwa Yohane, nati kwa iye, Rabi, Iye amene anali ndi inu tsidya lija la Y ordano, amene munamcitira umboni, taonani yemweyu abatiza, ndipo anthu onse alinkudza kwa iye.

27. Yohane anayankha nati, Munthu sakhoza kulandira kanthu, ngati sikapatsidwa kwa iye kocokera Kumwamba.

Werengani mutu wathunthu Yohane 3