Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 21:17-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ananena: naye kacitatu, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine? Petro anamva cisoni kuti anati kwa iye kacitatu, Kodi undikonda Ine? ndipo anati kwa iye, Ambuye, mudziwa Inu zonse; muzindikira kuti ndikukondani Inu. Yesu ananena naye, Dyetsa nkhosa zanga.

18. Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, pamene unali mnyamata unadzimangira wekha m'cuuno, ndipo unayenda kumene unafuna; koma pamene udzakalamba udzaturutsa manja ako, ndipo adzakumanga wina, nadzakunyamula kumene sufuna.

19. Koma ici ananena ndi kuzindikiritsa imfa imene adzalemekeza nayo Mulungu. Ndipo m'mene ananena ici, anati kwa iye, nditsate Ine,

20. Petro, m'mene anaceuka, anapenya wophunzira amene Yesu anamkonda alikutsata, amenenso anatsamira pacifuwa pace pamgonero, nati, Ambuye, ndani iye wakupereka Inu?

21. Pamenepo Petro pakumuona, ananena kwa Yesu, Ambuye, koma nanga uyu?

Werengani mutu wathunthu Yohane 21