Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 20:15-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Yesu ananena naye, Mkazi, uliranji? ufuna yani? Iyeyu poyesa kuti ndiye wakumunda, ananena ndi iye, Mbuye ngati mwamnyamula iye, ndiuzeni kumene mwamuika iye, ndipo ndidzamcotsa.

16. Yesu ananena naye, Mariya. Iyeyu m'mene anaceuka, ananena ndi iye m'Cihebri, Raboni; cimene cinenedwa, Mphunzitsi.

17. Yesu ananena naye, Usandikhudze, pakuti sindinatha kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kunka kwa Atate wanga, ndi Atate wanu, ndi Mulungu wanga, ndi Mulungu wanu.

18. Mariya wa Magadala anapita nalalikira kwa akuphunzirawo, kuti, Ndaona Ambuye; ndi kuti ananena izi kwa iye.

19. Pamenepo, pokhala madzulo, tsiku lomwelo, loyamba la Sabata, makomo ali citsekere, kumene anakhala akuphunzira, cifukwa ca kuopa Ayuda, Yesu anadza naimirira pakati pao, nanena nao, Mtendere ukhale ndi inu.

20. Ndipo pamene adanena ici, anaonetsa iwo manja ace ndi nthiti zace. Pamenepo akuphunzira anakondwera pakuona Ambuye.

21. Cifukwa cace Yesu anatinso kwa iwo, Mtendere ukhale ndi inu; monga Atate wandituma Ine, Inenso ndituma inu.

Werengani mutu wathunthu Yohane 20