Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 19:33-42 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. koma pofika kwa Yesu, m'mene anamuona iye, kuti wafa kale, sanatyola miyendo yace;

34. koma mmodzi wa asilikari anamgwaza ndi nthungo m'nthiti yace, ndipo 2 panaturuka pomwepo mwazi ndi madzi.

35. Ndipo 3 iye amene anaona, wacita umboni, ndi umboni wace uti woona; ndipo iyeyu adziwa kuti anena zoona, kuti inunso mukakhulupire.

36. Pakuti izi zinacitika, kuti lembo likwaniridwe, 4 Pfupa la iye silidzatyoledwa.

37. Ndipo linenanso lembo lina, 5 Adzayang'ana pa iye amene anampyoza.

38. 6 Citatha ici. Y osefe wa ku Arimateya, ndiye wophunzira wa Yesu, koma mobisika, cifukwa ca kuopa Ayuda, anapempha Pilato kuti akacotse mtembo wa Yesu. Ndipo Pilato analola. Cifukwa cace anadza, nacotsa mtembo wace.

39. Koma anadzanso 7 Nikodemo, amene anadza kwa iye usiku poyamba paja, alikutenga cisanganizo ca mure ndi aloe, monga miyeso zana.

40. Pamenepo anatenga mtembo wa Yesu, nauzenenga ndi nsaru zabafuta pamodzi ndi zonunkhira, monga mwa maikidwe a maliro a Ayuda.

41. Koma kunali munda kumalo kumene anapacikidwako, ndi m'mundamo munali manda atsopano m'mene sanaikidwamo munthu ali yense nthawi zonse.

42. 8 Pomwepo ndipo anaika Yesu, cifukwa ca tsiku lokonzera la Ayuda, pakuti mandawo anali pafupi.

Werengani mutu wathunthu Yohane 19