Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 19:31-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Pomwepo Ayuda, popeza panali tsiku lokonzera, kuti 1 mitembo ingatsale pamtanda tsiku la Sabata, pakuti tsiku lomwelo la Sabata linali lalikuru, anapempha Pilato kuti miyendo yao ityoledwe, ndipo acotsedwe.

32. Cifukwa cace anadza asilikari natyola miyendo ya woyambayo, ndi ya winayo wopacikidwa pamodzi ndi iye;

33. koma pofika kwa Yesu, m'mene anamuona iye, kuti wafa kale, sanatyola miyendo yace;

34. koma mmodzi wa asilikari anamgwaza ndi nthungo m'nthiti yace, ndipo 2 panaturuka pomwepo mwazi ndi madzi.

35. Ndipo 3 iye amene anaona, wacita umboni, ndi umboni wace uti woona; ndipo iyeyu adziwa kuti anena zoona, kuti inunso mukakhulupire.

36. Pakuti izi zinacitika, kuti lembo likwaniridwe, 4 Pfupa la iye silidzatyoledwa.

Werengani mutu wathunthu Yohane 19