Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 19:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo tsono Pilato anatenga Yesu, namkwapula.

2. Ndipo asilikari, m'mene analuka korona waminga anambveka pamutu pace, nampfunda iye maraya acibakuwa;

3. nadza kwa iye, nanena, Tikuoneni, Mfumu ya Ayuda! nampanda khofu.

4. Ndipo Pilato anaturukanso kunja, nanena nao, Taonani, ndidza naye kwa inu kunja kuti mudziwe kuti sindipeza mwa iye cifukwa ciri conse.

5. Pamenepo Yesu anaturuka kunja, atabvala korona waminga; ndi maraya acibakuwa, Ndipo ananena nao, Taonani munthuyu!

6. Ndipo pamene ansembe akulu ndi anyamata anamuona iye, anapfuula nanena, Mpacikeni, mpacikeni, Pilato ananena nao, Mtengeni iye inu nimumpaeike; pakuti ine sindipeza cifukwa mwa: iye.

7. Ayuda anamyankha iye, Tiri naco cilamulo ife, ndipo monga mwa cilamuloco ayenera kufa, cifukwa anadziyesera Mwana wa Mulungu.

8. Ndipo pamene Pilato anamva mau awa, anaopa koposa.

9. Ndipo analowanso ku Pretorio, nanena kwa Yesu, Mucoka kuti? koma Yesu sanamyankha kanthu.

Werengani mutu wathunthu Yohane 19