Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 18:37-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

37. Pamenepo Pilato anati kwa iye, Nanga kodi ndiwe Mfumu? Yesu anayankha, Munena kuti ndine Mfumu. Ndinabadwira ici Ine, ndipo ndinadzera ici kudza ku dziko lapansi, kuti ndikacite umboni ndi coonadi. Yense wakukhala mwa coonadi amva mau anga.

38. Pilato ananena kwa iye, Coonadi nciani? Ndipo pamene adanena ici, anaturukiranso kwa Ayudawo, nanena nao, vine sindipeza konse cifukwa mwa iye.

39. Koma muli nao makhalidwe, akuti ndimamasulira inu mmodzi pa Paskha; kodi mufuna tsono kuti ndimasulire inu Mfumu ya Ayuda?

40. Pomwepo anapfuulanso, nanena, Si uyu, koma Baraba. Koma Baraba anali wacifwamba.

Werengani mutu wathunthu Yohane 18