Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 18:31-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Ndipo Pilato anati kwa iwo, Mumtenge iye inu, ndi kumweruza iye monga mwa cilamulo canu. Ayuda anati kwa iye, Tiribe ulamuliro wakupha munthu ali yense;

32. kuti mau a Yesu akwaniridwe, amene ananena akuzindikiritsa imfa imene, akuti adzafa nayo.

33. Cifukwa cace Pilato analowanso m'Pretorio, naitana Yesu, nati kwa iye, Iwe ndiwe Mfumu ya Ayuda kodi?

34. Yesu anayankha, Kodi munena ici mwa inu nokha, kapena ena anakuuzani za Ine?

35. Pilato anayankha, ndiri ine Myuda kodi? Mtundu wako ndi ansembe akulu anakupereka kwa ine; wacita ciani?

36. Yesu anayankha, Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi; ufumu wanga ukadakhala wa dziko lino lapansi, anyamata anga akadalimbika nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga suli wocokera konkuno.

37. Pamenepo Pilato anati kwa iye, Nanga kodi ndiwe Mfumu? Yesu anayankha, Munena kuti ndine Mfumu. Ndinabadwira ici Ine, ndipo ndinadzera ici kudza ku dziko lapansi, kuti ndikacite umboni ndi coonadi. Yense wakukhala mwa coonadi amva mau anga.

38. Pilato ananena kwa iye, Coonadi nciani? Ndipo pamene adanena ici, anaturukiranso kwa Ayudawo, nanena nao, vine sindipeza konse cifukwa mwa iye.

39. Koma muli nao makhalidwe, akuti ndimamasulira inu mmodzi pa Paskha; kodi mufuna tsono kuti ndimasulire inu Mfumu ya Ayuda?

40. Pomwepo anapfuulanso, nanena, Si uyu, koma Baraba. Koma Baraba anali wacifwamba.

Werengani mutu wathunthu Yohane 18