Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 18:19-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo mkulu wa ansembe anafunsa Yesu za akuphunzira ace, ndi ciphunzitso cace.

20. Yesu anayankha iye, Ine ndalankhula zomveka kwa dziko lapansi; ndinaphunzitsa Ine nthawi zonse m'sunagoge ndi m'Kacisi, kumene amasonkhana Ayuda onse; ndipo mobisika sindinalankhula kanthu.

21. Undifunsiranji Ine? funsa iwo amene adamva cimene ndinalankhula nao; taona, amenewo adziwa cimene ndinanena Ine.

22. Koma m'mene iye adanena izi, mmodzi wa anyamata akuimirirako anapanda Yesu khofu, ndi kuti, Kodi uyankha mkulu wa ansembe comweco?

23. Yesu anayankha iye, Ngati ndalankhula coipa, cita umboni wa coipaco, koma ngati bwino, undipandiranji?

24. Koma Anasi adamtumiza iye womangidwa kwa Kayafa mkulu wa ansembe.

25. Koma Simoni Petro analikuimirira ndi kuotha moto. Pomwepo anati kwa iye, Suli iwenso wa akuphunzira ace kodi? Iyeyu anakana, nati, Sindine.

26. Mmodzi wa akapolo a mkulu wa ansembe ndiye mbale wace wa uja amene Petro anamdula khutu, ananena, Ine sindinakuona iwe kodi m'munda pamodzi ndi iye?

27. Pamenepo Petro anakananso; ndipo pomwepo analira tambala.

28. Pamenepo anamtenga Yesu kucokera kwa Kayafa kupita ku Pretorio; koma munali mamawa; ndipo iwo sanalowa ku Pretorio, kuti angadetsedwe, koma kuti akadye Paskha.

29. Cifukwa cace Pilato anaturukira kunja kwa iwo, nati, Cifukwa canji mwadza naco ca munthu uyu?

30. Anayankha nati kwa iye, Akadakhala wosacita zoipa uyu sitikadampereka iye kwa inu.

31. Ndipo Pilato anati kwa iwo, Mumtenge iye inu, ndi kumweruza iye monga mwa cilamulo canu. Ayuda anati kwa iye, Tiribe ulamuliro wakupha munthu ali yense;

32. kuti mau a Yesu akwaniridwe, amene ananena akuzindikiritsa imfa imene, akuti adzafa nayo.

Werengani mutu wathunthu Yohane 18