Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 16:5-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Koma tsopano ndimuka kwa iye wondituma Ine; ndipo palibe wina mwa inu andifunsa Ine, Munka kuti?

6. Koma cifukwa ndalankhula izi ndi inu cisoni cadzala mumtima mwanu.

7. Koma ndinena Ine coonadi ndi inu; kuyenera kwa inu kuti ndicoke Ine; pakuti ngati sindicoka, Nkhosweyo sadzadza kwa inu; koma ngati ndipita ndidzamtuma iye kwa inu.

8. Ndipo atadza Iyeyo, adzatsutsa dziko lapansi za macimo, ndi za cilungamo, ndi za ciweruziro;

9. za macimo, cifukwa sakhulupirira Ine;

10. za cilungamo, cifukwa ndinka kwa Atate, ndipo simundionanso;

11. za ciweruziro, cifukwa mkuru wa dziko ili lapansi waweruzidwa.

12. Ndiri nazo zambirinso zakunena kwa inu, koma simungathe kuzisenza tsopano lino.

13. Koma atadza Iyeyo, Mzimu wa coonadi, adzatsogolera inu m'coonadi conse; pakuti sadzalankhula za iye mwini; koma zinthu ziri zonse adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zirinkudza adzakulalikirani.

14. Iyeyo adzalemekeza Ine; cifukwa adzatenga za mwa Ine, nadzalalikira kwa inu.

15. Zinthu ziri zonse Atate ali nazo ndi zanga; cifukwa cace ndinati, kuti atenga za mwa Ine, nadzalalikira kwa inu.

Werengani mutu wathunthu Yohane 16