Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 16:19-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Yesu anazindikira kuti analikufuna kumfunsa iye, ndipo anati kwa iwo, Kodi mulikufunsana wina ndi mnzace za ici, kuti ndinati, Kanthawi ndipo simundiona Ine, ndiponso kanthawi nimudzandiona Ine?

20. Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mudzalira ndi kubuma maliro inu, koma dziko lapansi lidzakondwera; mudzacita cisoni inu, koma cisoni canu cidzasandulika cimwemwe.

21. Mkazi pamene akuti abale ali naco cisoni, cifukwa yafika nthawi yace; koma pamene wabala mwana, sakumbukilanso kusaukako, cifukwa ca cimwemwe kuti wabadwa munthu ku dziko lapansi.

22. Ndipo inu tsono muli naco cisoni tsopano lino, koma ndidzakuonaninso, ndipo mtima wanu udzakondwera, ndipo palibe wina adzacotsa kwa inu cimwemwe canu.

23. Ndipo tsiku limenelo simudzandifunsa kanthu. Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Ngati mudzapempha Atate kanthu, adzakupatsani inu m'dzina langa.

Werengani mutu wathunthu Yohane 16