Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 16:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Izi ndalankhula ndi inu kuti mungakhumudwitsidwe.

2. Adzakuturutsani m'masunagoge; koma ikudza nthawi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikira Mulungu,

3. Ndipo izi adzacita, cifukwa sanadziwa Atate, kapena Ine.

4. Koma zinthu izi ndalankhula ndi inu kuti ikadza nthawi yao, mukakumbukire kuti ndinakuuzani. Koma izi sindinanena kwa inu kuyambira paciyambi, cifukwa ndinali pamodzi ndi inu.

5. Koma tsopano ndimuka kwa iye wondituma Ine; ndipo palibe wina mwa inu andifunsa Ine, Munka kuti?

6. Koma cifukwa ndalankhula izi ndi inu cisoni cadzala mumtima mwanu.

7. Koma ndinena Ine coonadi ndi inu; kuyenera kwa inu kuti ndicoke Ine; pakuti ngati sindicoka, Nkhosweyo sadzadza kwa inu; koma ngati ndipita ndidzamtuma iye kwa inu.

8. Ndipo atadza Iyeyo, adzatsutsa dziko lapansi za macimo, ndi za cilungamo, ndi za ciweruziro;

9. za macimo, cifukwa sakhulupirira Ine;

10. za cilungamo, cifukwa ndinka kwa Atate, ndipo simundionanso;

11. za ciweruziro, cifukwa mkuru wa dziko ili lapansi waweruzidwa.

12. Ndiri nazo zambirinso zakunena kwa inu, koma simungathe kuzisenza tsopano lino.

Werengani mutu wathunthu Yohane 16