Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 13:26-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Ndipo Yesu anayankha, Ndi iyeyu, amene Ine ndidzamsunsira nthongo ndi kumpatsa, Pamenepo, m'mene anasunsa nthongo anaitenga naipatsa Yudase mwana wa Simoni Isikariote.

27. Ndipopambuyo pace pa nthongoyo, Satana analowa mwa iyeyu. Pamenepo Yesu ananena naye, Cimene ucita, cita msanga,

28. Kama palibe mmodzi wa iwo akuseamako anadziwa cimene anafuna, poti atere naye.

29. Pakuti popeza Yudase anali nalo thumba, enaanalikuyesakuti Yesu ananena kwa iye, Gula zimene zitisowa paphwando; kapena, kuti apatse kanthu kwa aumphawi.

30. Pamenepo iyeyo m'mene adalandira nthongo, anaturuka pomwepo, Koma kunali usiku.

31. Tsono m'mene adaturuka, Yesu ananena, Tsopano walemekezeka Mwana wa munthu, ndipo Mulungu walemekezedwa mwa iye;

32. ndipo Mulungu adzamlemekeza iye mwa iye yekha, adzamlemekeza iye tsopano apa.

33. Tiana, katsala kanthawi ndikhala ndi inu. Mudzandifunafuna Ine; ndipo monga ndinanena kwa Ayuda, kuti kumene ndinkako Ine, inu simungathe kudza, momwemo ndinena kwa inu tsopano.

34. Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzace; monga ndakonda Inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzace.

35. 1 Mwa ici adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli naco cikondano wina ndi mnzace.

Werengani mutu wathunthu Yohane 13