Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 13:21-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Yesu m'mene adanenaizi, anabvutika mumzimu, nacita umboni, nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mmodzi wa inu adzandipereka Ine.

22. Akuphunzira analikupenyanawina kwa mnzace, ndi kusinkhasinkha kuti ananena za yani.

23. Koma mmodzi wa akuphunzira ace, amene Yesu anamkonda, analikutsamira pa cifuwa ca Yesu.

24. Pamenepo Simoni Petro anamkodola nanena naye, Utiuze ndiye yani amene anena za iye.

25. Iyeyu potsamira pomwepo, pa cifuwa ca Yesu, anena ndi iye. Ambuye, ndiye yani?

26. Ndipo Yesu anayankha, Ndi iyeyu, amene Ine ndidzamsunsira nthongo ndi kumpatsa, Pamenepo, m'mene anasunsa nthongo anaitenga naipatsa Yudase mwana wa Simoni Isikariote.

27. Ndipopambuyo pace pa nthongoyo, Satana analowa mwa iyeyu. Pamenepo Yesu ananena naye, Cimene ucita, cita msanga,

28. Kama palibe mmodzi wa iwo akuseamako anadziwa cimene anafuna, poti atere naye.

29. Pakuti popeza Yudase anali nalo thumba, enaanalikuyesakuti Yesu ananena kwa iye, Gula zimene zitisowa paphwando; kapena, kuti apatse kanthu kwa aumphawi.

30. Pamenepo iyeyo m'mene adalandira nthongo, anaturuka pomwepo, Koma kunali usiku.

31. Tsono m'mene adaturuka, Yesu ananena, Tsopano walemekezeka Mwana wa munthu, ndipo Mulungu walemekezedwa mwa iye;

32. ndipo Mulungu adzamlemekeza iye mwa iye yekha, adzamlemekeza iye tsopano apa.

33. Tiana, katsala kanthawi ndikhala ndi inu. Mudzandifunafuna Ine; ndipo monga ndinanena kwa Ayuda, kuti kumene ndinkako Ine, inu simungathe kudza, momwemo ndinena kwa inu tsopano.

34. Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzace; monga ndakonda Inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzace.

35. 1 Mwa ici adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli naco cikondano wina ndi mnzace.

36. Simoni Petro anena ndi iye, Ambuye, mumuka kuti? Yesu anayankha, Kumene ndimukako sungathe kunditsata Ine tsopano; koma, 2 udzanditsata bwino lomwe.

37. Petro ananena ndi iye, Ambuye, sindingathe kukutsatani Inu tsopano cifukwa ninji? 3 Ndidzataya moyo wanga cifukwa ca Inu.

38. Yesu anayankha, Moyo wako kodi udzautaya cifukwa ca Ine? Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Asanalire tambala udzandikana Ine katatu.

Werengani mutu wathunthu Yohane 13